Sports

“Tiyichinyira kumbuyo lero Cameroon ndipo palibenso zopemphera,” atero a Malawi ena

Malawi ikuyesetsa kuti ipite nawo ku masewera a AFCON ndipo a Nyamilandu akuti Malawi ndi Barcelona yaku Africa

Week yatha pomwe Malawi inakumana ndi Cameroon ku dziko lawo, a Malawi ambiri anali okhumudwa ndizotsatira za masewerawo omwe anathera chigoli chimodzi kwa chete chete kupangitsa Cameroon kukhala otsogula mu gulu lachiwiri la AFCON.

Anthu ambiri analiso okhumudwa kamba koti timu ya Flames inayika nthawi yambili mumapemphero ofunsa kuwina kwa ambuye m’malo mokozekera kuthupi.

Koma pomwe Cameroon ili mu dziko lino ndipo ikumenya ndi Flames lero pakwawo pa Chichiri Stadium, anthu ambiri kuphatikizapo coach wa team iyi bambo RVG ati Cameroon iwonetsedwa chomwe chinameta nkhanga mpala lero ndipo idziwa chomwe Malawi amayitchulira kuti ‘malawi a moto.’

M’modzi mwa a Malawi osapota timu yathu a Aubrey Malunga ati Cameroon ayipanga zoopsa. Iwo anati Flames iwachinyira kumbuyu anyamata a Cameroon ndipo apita kwawo nkhope zili zo zyolika ndi manyazi. Iwo amatanthawuza kuti Flames isewera mbali imodzi ya akwadani powapanikiza ndi mpira.

Inu mukuganiza bwanji? Gawiraniko ena nkhaniyi kuti nawo apereke maganizo awo.

Anyamata a Cameroon
Tags
Show More

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Close